20/04/2024
NKHWAZI PA M'BAWA
Monga momwe mbendera ya dziko la Malawi ili ndi dzuwa lotuluka,tinene pano kuti chaka china m'buyomu dzuwal lidasinthidwa kukhala lowala moswa mtengo,kumbuyo kwake kuli mitundu yakuda kuimila anthu ake,wofiyila ndiye magazi a akuluakulu omwe akhala akumenyela ufulu wathu,wobiliwila ndiye chilengedwe .nafeso bwanji tikhale nayo mbendera iziwuluka petupetu pambali pa yafukoyi.kodi ikhale yamtundu wanji?ndiye fuso.mwina yoyela mbu kapena yobiliwila ngati mtambo kuimilila madzi a mumtsinje wa Nafisi,adzina athu, ndi nkhwazi pa m'bawa .osati ndife mfumu ya nyumba zogona apaulendo ayi koma kungofuna kulemekeza mayi chilengedwe potipatsa zosowa zathu moolowa manja nthawi zose.mwachidule tikhoza kungoti kamnafisi adamangidwa pa nkhalango,poti padali mtengo waukulu wa m'bawa omwe umkakodola chikoka cha mbalame mtundu ose.udamela okha m'bali mwa mtsinje wa Nafisi pafupi ndi ulalo wa njanje pa dziwe lotchedwa Chidinti pomwe amayi amakonda kuchapa ndi ana kusambila;mtengowu udatipatsa maganizo odzala mitengo ina yambili pafupi pake yomwe idakula mkukhala nkhalango yowilila yomwe ikadalipo mpaka lelo.ndipo idatithandiza kuotcha njerwa zomwe tidamangila makoma athu,kukoza akatawala okwelapo amisili omanga nyumba,kufolela denga,kukhoma mazenela,zitseko ndi makama.nkhuni zake ndizomwe timaphikila kadaundamadzi,ndikuphitsa thiyi kukamtini wathu,komaso kuteleka madzi ogaduka bwino,osamba alendo athu.pophelanphongo abale ndi alongo tiyeni tidzale mitengo sidzatikhumudwitsa ayi koma ubwino wake ngosasimbika ndipo mwina ndi yomwe adzatinyamulile tikadzafa.