05/11/2023
Adzukulu a m'mudzi wa Sawasawa mdera la mfumu yaikulu Nanseta ku Thyolo akakamiza akuluakulu a mpingo wa Apostolic Faith kunyamula ndi kuika okha maliro a msungwana yemwe wamwalira poganizira kuti sanapite naye ku chipatala kamba kachikhulupiliro cha mpingowu.
Malinga ndi phunzitsi wina wa sukulu ya pulaimale ya Mikombe mderalo, msungwanayu yemwe anali sitandade 5 anagwa ndi kukomoka dzulo akuphunzira phunziro la zaluso.
Koma makolo ake atabwera kumutenga, zikumveka kuti sanapite naye ku chipatala kaamba ka chikhulupiliro cha mpingowu ndipo wamwalira usiku wa dzulo.
Izi zinakwiitsa mafumu ndi adzukulu omwe ati ananyanyalira mwambo onse wamaliro akuluakulu a mpingowu ponena kuti mayi awo a malemuwa anamwaliranso miyezi iwiri yapitayo atadwala koma osalandira thandizo la chipatala.
(by Luka Beston - Thyolo: 11/03/2023)